Rosemary Tembo
Organisation BSM
Country Malawi
Region Central Africa
Sector Lifelong Learning
Position/Job title Assistant Literacy Coordinator
My experience in adult learning and education
Akulu akulu nthawi zambiri amaphunzira ndi cholinga, amakhala ndi Chidwi kuti chomwe akufuna kuphunzira achidziwe, amafuna kulemekezedwa komanso amafuna muwathandize kuchoka ku zomwe amadziwa kufika ku zinthu zomwe sakudziwa. Munthu wamkulu safuna kukalipidwa, amasatira zinthu pena mwachangu ndipo ena mochedwa koma onsewa amafunikira kuti muyende ndi kuwathandizira limodzi malingana ndi kuthekera kwao. Amenewa amasiyana ndi ana choncho mphunzitsi asamawatenge ngati ndi ana. Sukulu simatha akulu akulu amaphunzira pena Poona, kulemba komanso kuchita nawo. Kuphunzira kwao kumafunikiranso masangulutso kuti socially azikhala olumbikitsika komanso mentally alert.